Madyedwe A Machiritso

Madyedwe A Machiritso

Share

Chakudya chanu nthawi zonse chizikhala mankhwala ndipo mankhwala anu odalirika azikhala chakudya!

30/07/2026

CHIMERA CHA TCHANA
✓Kwa inu amene mukudziwa TCHANA mundimvomereza kuti ndi chakudya chabwino.
✓Amakazinga ndi kudya monga muja tidya mtedza okazinga.
✓Tchanatu amapanganso chimera ndipo ndiwo zabwino zedi!
✓Kumeretsa tchana ndi kofunika zedi pochitsa "phytic acid" yemwe amabweretsa mavuto mmimba koma shuga otchedwa kuti "oligosaccharides" yemwe amapenzeka mu zakudya za banja la nyemba, ndipo amasisimitsa mnyembazo mmimba zomwe zimapangitsa mpweya wammimba.
✓Chonch kumeretsa kaye nyemba musanaphike ndi chinthu chofunikira zedi.
✓Chimera cha tchana chiri ndi mlingo waukuru wa iron. Izi zikutanthauza kuti chikhoza kukhala chakudya chabwino zedi cha anthu omwe akuchepekedwa magazi.
✓Icho chirinso ndi folate ochuruka yemwe ndi ofunikira zedi m'thupi la munthu yemwe akuvutika ndi "Sickle cell anaemia."
✓Tchana chomeretsa chiri ndi ma B vitamins, vitamins A ndi C.
✓Icho chirinso ndi protein wabwino zedi.

Chithunzi mukuchionachi ndi chachimera cha tchana chomwe tapanga kunoku. Masiku atatu chatheka ndipo sichivuta kupanga!

27/07/2026

Big shout out to my newest top fans! Lyton Malunga, Jenefer Lupapa, Groly Jabu, M***a Hella, Esther Malemia

24/07/2026

MALABAR CHEST NUTS
✓Ambiri akuti umawapangitsa nseru ndipo umawasazitsa.
✓Ambiri amadya mtedza uwu kwachabe osatsata malangizo
✓Mtedza uwu umayenera kuphikidwa kapena kukazinga kaye musanadye
✓Osadya opitirira 15 patsiku
✓Ana osapitirira zaka ziwiri asadye wathuthu koma muchite kusinja ndi kumawayikira m'mphala
✓Ana azaka zisanu kufikira 10 omwe ndi onyentchera komanso osalemera adzipatsidwa uwiri kapena utatu kuti adye masiku atatu pa mlungu.
✓Mtedza umenewu umasunjidwa ndi kupangira nsinjiro zabwino zedi. Tsirani mu ndiwo zanu pa mlingo wabwino. Osachurukitsa.
✓Mtedza uwu amaonjenzera mnyonga m'thupi. Choncho aja mumadandaula ndi kuchepekedwa mnyonga aja pezani mtedza umenewu muzidya.
✓Iwotu uli ndi Vitamin E, komanso Omega-9 fatty acids omwe amathandiza kuti ubongo ukhale wa thanzi labwino komanso uzitha kukumbukira zinthu
✓Mafuta amenewa amathandizanso kuonjenzera thanzi labwino la mtima
✓Uli ndi mlingo wabwino wa iron ndi copper omwe amathandiza kupanga magazi m'thupi.
✓Uli ndi mlingo wabwino wa potassium yemwe amathandiza kutsitsa BP.
✓Uli ndi Calcium, komanso magnesium omwe amathandiza kulimbitsa mafupa
✓Mtedzawutu umakuzanso chitetezo cha matenda m'thupi.
✓Umatseka kutsegula mmimba. Pangani tiyi pogwiritsa ntchito ufa wa mtedza umenewu okazinga.

Ndakuuzani momveka bwino. Usiku wabwino.

Photos from Madyedwe A Machiritso's post 24/07/2026

Nkhungudzu
✓Ndiwo izi zimafunika kuphika kwambiri kuti Ka poizoni komwe kamakhala mmakoko mwake kafe
✓Zikapsya bwino ziyenera kutsiridwa nsinjiro, tomato, anyezi ndi mlingo woyenera wa mchere.
✓Ndiyetu ndi ndiwo zabwino zedi zopatsa thanzi.
✓Anthu amene akudwala nthenda ya shuga ndi ndiwo zabwino zothandiza kuti mlingo wa shuga wa mmagazi usakwere.
✓Zimathandizanso kuthana ndi vuto la kudzimbidwa.
✓Ndi zabwino zedi pa thanzi labwino la mtima.
✓Zimapereka thanzi labwino ku chigayo cha zakudya m'thupi!

17/07/2026

CHIMANGA CHOFIIRA
✓Chimanga ichi ichi ndi lokolo weniweni ndipo ndi chabwino zedi.
✓Kufiirako musadabwe ndi chionetsero cha kuchuruka kwa ma "Anthocyanins" komanso "Lutein."
✓"Anthocyanins?" Eya. Awatu ndi ma "Phytochemicals" omwe ndi ofunikira zedi pa nkhani ya kuteteza ndi kulimbana ndi tizirombo toyambitsa khansa! Kodi inu mwatero? Eya ifeyo tikutero!
✓Ma "Anthocyanins" amakuzanso chitetezo cha matenda m'thupi komanso ndi ofunikira zedi m'thupi la munthu yemwe akuvutika ndi nthenda ya shuga.
✓Ndiyetu chimanga ichi ndi chofunika zedi! Inde kaya.
✓Ichotu chimathandizansotu kutsitsa BP, kupereka thanzi labwino la mtima komanso kuletsa ukalamba!
✓Akutitu ndi chophikira thobwa! Nkhani zaketu zikutero. Thobwa lake labwino zedi loti kumwa madzulo basi osadyando nsima iwe ndi kukagona zabwino bwino ndithu.
✓Ndiyetu sitikuimira pamenepo. Chimagachi mukhoza kuphika nsima, chigumu, komanso kusakaniza ndi ufa wa zinthu zina kupangira zakudya zopatsa thanzi!

✓Chaka chino chokha mulime. Mbeu ikupezeka ndi a Eden Green Nursery and Food Forests Ku Ntcheu pa Boma.
K5000 per kg.
0991183538.

Photos from Madyedwe A Machiritso's post 08/07/2026

NDIWO ZA MASAMBA A MPINIMBI
✓Ndikudziwa kuti izi ndi zachilendo mwina ambiri simukudziwa kuti masamba a mpinimbi amakhoza kuphikidwa ndipo mukhoza kudyera nsima kapena mphunga.
✓Anthu a ku Nigeria amaphika ndipo amasakaniza ndi zakudya zina.
✓Ngati mtengowu simukudziwa chonde musayerekeze kutenga masamba ndi kuphika ngati ndiwo kuopa kuti mungagwiritse ntchito mtengo omwe sindiwo.
✓Masamba amene amafunikira ndi ophukira kumene osati okhwima. Mwina ndinene kuti a nkhanda.
✓Masambawo amawawira pang'ono koma vutolo limathetsedwa potsira nsinjiro, tomato, anyezi ndi mchere.
✓Poyamba mumatenga masamba athlete kapena ankhanda a mtengo wa mpinimbi ndi kuwatsuka bwino; penanso ndi madzi otentha.
✓Kenako phikani masambawo monga muchitira ndi ndiwo zina za masamba.
✓Kenako tsirani nsinjiro, tomato, anyezi ndi mchere ndipo takasani.
✓Dikirani pang'ono ndipo kenako mukhoza kuphula.

✓Mukhoza kudyera nsima kapena mpunga.
✓Ziri ndi ma vitamins monga vitamin A, C komanso michere monga Calcium, iron, Copper ndi magnesium.
✓Ndizothandiza kwa anthu omwe ali ndi mavuto a mmimba, anthu amene BP ndi yokwera, anthu ochepekedwa magazi, komanso anthu amene ali ndi mavuto okhudzana ndi kuphwanya kwa thupi. Ndiwozi zimatha kuziziritsa ululu.

EDEN GREEN NURSERY AND FOOD FOREST IN NTCHEU
0991183538

Photos from Madyedwe A Machiritso's post 08/07/2026

MPINIMBI
✓Ndiyetu zipatso zimenezi ziri ndi mlingo wabwino wa Omega-3 fatty acids komanso Omega-6 fatty acids.
✓Awati ndi mafuta abwino zedi amene amathandiza thanzi labwino la mtima, ubongo, m'mitsempha ya magazi komanso chiwindi.
✓Kuonjenzera apo zipatsozi ziri ndi mlingo waukuru wa fiber. Choncho ndi zothandiza kuonjenzera thanzi labwino la chifu komanso matumbo akuru. Zimathandiza kuti chiwerengero cha ma bacteria abwino m'thumbo lalikuru chikwere zomwe ndi zothandiza kuteteza matenda osiyana siyana kuphatikizapo matenda a shuga.

Ife a Eden Green Nursery and Food Forests kuno ku Ntcheu tikhala tikukupatsirani zambiri zokhudzana ndi Mpinimbi, Mahuhu ndipo ena akuti Mtonongoli.

EDEN GREEN NURSERY AND FOOD FOREST IN NTCHEU
0991183538

Photos from Madyedwe A Machiritso's post 08/07/2026

MALABAR CHEST NUTS
✓Mawa wa lero ndalandira parcel imeneyi kuchokera kwa mmodzi otsatira tsamba lino wa ku Mchinji.
✓Iye, zaka zambuyomu anagula mitengo 4 ya mtedza umenewu, yomwe omugulitsayo anati ndi "Brazilian Nuts."
✓Koma kupyolera pa search yake pa makina a internate anapeza kuti mtedza uwu si Brazilian Nuts. Izi zimachitika pomwe mitengo yake inayamba kubereka.
✓Ndiye sanachedwe koma kufufuza ku Eden Green Nursery kuti kodi mtedza umenewu ndi wanji.
✓Ndipo ndinawatsikimizira kuti umenewu ndi "Malabar Chest nuts!"
✓Ndiye ananditsikimizira kuti tsiku lomwe alowe mu tawuni ya Lilongwe akatumiza; ndipo achitadi moteromo!
✓Kodi inuyo mukudziwa kuti kunja kuno kulinso mtedza umenewu?
✓Kodi mukudziwa kuti mtengo wa Malabar Chest nut ndi okongola zedi?
✓Nanga alipo pano ena omwe ali nawo?

EDEN GREEN NURSERY AND FOOD FOREST IN NTCHEU
0991183538

Photos from Madyedwe A Machiritso's post 06/07/2026

MPINIMBI, MDYANKHANDWE, MAHUHU, MTONONGOLI
✓Mainawo akutero
✓Zipatso zidetsa mano izi
✓Zimathandizira kupanga moyo wakumudzi kukhala okoma zedi.
✓Mitengo yake imapezeka m'tchire ndipo ndi yachilengedwe
✓Zipatsozi zikapya bwino zimayiyoka zokha mu mtengo ndipo timachita kutola pansi.
✓Timadya zaziwisi, kapena kuphika kapena zikhozanso kuumitsidwa kumene.
✓Zipatso izizi izi ndi zabwino zedi pa thanzi la munthu.
✓Kudako osakudabwa ayi ndi kuchurukidwa kwa ma "Anthocyanins."
✓Kumbukirani kuti ma "Anthocyanins" amateteza thupi Ku khansa, kutsitsa BP, kuteteza matenda a mtima komanso matenda a shuga.
✓Zirinsotu ndi mlingo waukuru wa vitamin A ndi vitamin C. Choncho limakuuza chitetezo cha matenda m'thupi komanso kuonjenzera thanzi labwino la maso.
✓Izo zirinso ndi B Vitamins monga Vitamin B1 ndi B6. Vitamin B6 amathandiza kuti mtima uzigunda moyenera.
✓Zirinso ndi michere monga Calcium, iron, potassium ndi zinc. Choncho ndiyofunikira pa thanzi labwino la mafupa.

Nthawi yakwana pomwe mitengo ngati iyi ikuguluka m'tchiremu, tiyambe kudzala mmakomo mwathu.

Osayiwala kuti akukupatsirani za thanzi patsamba lino ndi a Eden Green Nursery ku Ntcheu.
EDEN GREEN NURSERY AND FOOD FOREST IN NTCHEU
0991183538.

05/07/2026

✓Chimanga Chofiira chikanalipobe
✓Mukafuna mbeu musakhale chete
✓Eden Green Nursery ku Ntcheu ikugulitsa ndithu pa mtengo wa k5000 per kg
✓Kumbukirani kuti ife a Eden Green Nursery ku Ntcheu tikukupatsirani za thanzi pa tsamba lino kupyolera mu thandizo lomwe timapeza mukatigula malonda omwe tikusatsa.

EDEN GREEN NURSERY IN NTCHEU
0991183538

Want your business to be the top-listed Beauty Salon in Ntcheu?
Click here to claim your Sponsored Listing.

Category

Telephone

Website

Address


Ntcheu