Grace Milly Mtema

Grace Milly Mtema

Share

Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Grace Milly Mtema, Health/Beauty, Chiradzulu.

24/08/2026

KUBWEREZA ENA ADAFUNSA

KUPANGA BISCUIT RECIPE

ZOFUNIKA

8 teaspoon of milk
Two egg
1 kg flour
quarte rof sugar
Quarter of cookingoil

NJIRA YOPANGIRA BISCUITS

Tengani mkaka wanu ndi sugar phatikizani ndikuzitakasa mpaka sugar ayambe
kusungunuka.

Mukatero iswani madzira anu awiri aja ndi kuthira mu sugar wanu yemwe
waphatikizidwa kale ndi mkaka.

Osayiwara kutakasa kwambiri kuti ziphatikidzane bwino.

Zikayamba kuphatikidzana bwino yambani kuthira flour wanu uja pang'onopang'ono
kuti zilimbe.

Kumbukirani kuti 1kg yonse ya flour isathe ndikuthira
Zikayamba kulimba zatheka.

Mukatero yambani kuumba timipira size yomwe mukufuna.

mukamalidza yambani
kudiliza pogwilitsa ntchito botolo la cococola or ngati muli ndizodilidzira chapati
mukhodza kugwilitsa ntchito.

Timipira mukhodza kutenga tambular yanu kuti zikhare zadongosolo komaso
muziwumba pogwilitsa ntchito flour yemwe adasara uja kuti zisamate manja.

Mukamalidza yatsani mbaula.

Pakanini mafuta mupoto wanu womwe mukufuna kuphikiramo biscuits wanu.

Mpoto wanu ukhare ndichovindikira chifukwa maphikidwe anu akhara ngati muphikachigumu.

Ikani zomwe mwapanga zija mupoto wanu omwe mwapaka kale mafuta ikani
pamoto dikirani kwamphindi zosachepela15 then onani ngati atheka.

Kumbukirani kuti timadondo kapena mawu omwe amakhara pa biscuit ajaamayikidwa nthawi yomwe akudilidza komaso pali zidindo zake.

18/08/2026

akuterotu

26/07/2026

loud n clear

26/07/2026

we're going there

15/07/2026

LET'S MAKE TSABOLA

5 cups any fresh tsabola
2 teaspoon mild raja
3 teaspoon paprika
3table spoon vinegar
3 cloves garlic
1 big onion
½ cup cooking oil
2 teaspoon salt
Muyamba kutsuka tsabola wanu, kenako muduladula tima pieces ting'onoting'ono, kenako tengani poto wanu, ikamimo mafuta moto ukhale wa size usachuluke, kenako ikamo anyezi ndi garlic( muduladula small pieces, pamodzi ndi garlic Onyenya) kenako kutakasa bwinobwino kenako ikanimo ma spice anu ndikutakasa bwinobwino kenako muyikamo tsabola wanu kenako mumusiya kuti apse uko mukutasa mwa apo ndi apo. Kenako thiramo salt ndi vinegar wanu. Kenako takasani kuti alowerere bwinobwino . kenako muphura kuti azizire musapange pack otetha ngati ali ogulitsa..

Salt ndi vinegar a papa ateteza kuti asawonongeke msanga..

Zikomo

12/07/2026

HOMEMADE TOMATO SAUCE
15 medium tomatoes
2 cups of water
½ teaspoon salt
½ cup white sugar
3 tablespoon lemon 🍋

PROCESS YAKE
Mutenga tomatoes mudula ma pieces ang'ono kenako muyika mu poto ndikuthira madzi. Muvindikira kuti zibwateko ndithu mpka tomatoes apse. Kenako muphula ndikuyika mu basin, ndikuyanba kukanyanga kuti zikhale phalaphale and njere zonse zikhale pathunda. Kenako mutenga sefa .muzisefa kuti tichotse makoko komaso njere. Kenako mutenga zosefa zija muyika, mumpoto ndikuyika pamoto. Kuthiramo salt, sugar ndikuyanba kutakasa, moto usachuluke kwambiri mutakasa ndithu mpaka ziyamba kuoneka mwaphalaphala( thickness) kenako muthiramo lemon juice. Ndikutakasa kenako muziphula kudikira zizire.

Tomato sauce watheka.

09/07/2026

Ngat mukuvutika ndi chifuwa cha mphumu chifuwa chosatha chooses mtendere

Tapeza chinyumba chazila zila lake likhale losapsa loti mwangochosamo kumene pezani tokwanila ndithu
Semani mtengo wagwafa uja
Tengani nchere wamabulu

Mukasema ntengo wagwafa muziotcha pamoto zifike pamakala chimodzi maodzi zimakungwa za zamazilazo komanso nchere muukazinge .zonsezo zikapsa muzipere zifike paufa(kusakaniza zonsezo mozipsereza pamoto)

Zikatheka mutenge powder ameneyi muzinyambita kaya ndi spoon imodzi mwana mpaseni kaspoon kakangono

Chifuwa chimenechi chimatheramo ndipo inuo in shaa Allah simuzadwalanso ayi .ngat pali kufunsa funsani tikuyankhani sindikuziwa ngat zanveka.

07/07/2026

Amen

06/07/2026

kupita kopemphera kubwerako nyamakazi itathatu kkkkkkk

Photos from Grace Milly Mtema 's post 06/07/2026
Want your business to be the top-listed Beauty Salon in Chiradzulu?
Click here to claim your Sponsored Listing.

Category

Website

Address

Chiradzulu

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Grace Milly Mtema posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Subscribe

We will notify you when anything happens in Chiradzulu.